Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 21:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye;

16. pamenepo kudzali, tsiku lakugawira ana ace amuna cuma cace, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu.

17. Koma azibvomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lace la zace zonse; popeza iye ndiye ciyambi ca mphamvu yace; zoyenera woyamba kubadwa nzace.

18. Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wace, kapena mau a mai wace, wosawamvera angakhale anamlanga;

19. azimgwira atate wace ndi mai wace, ndi kuturukira naye kwa akuru a mudzi wace, ndi ku cipata ca malo ace;

20. ndipo anene kwa akulu a mudzi wace, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera.

21. Pamenepo amuna onse a mudzi wace amponye miyala kuti afe; cotero mucotse coipaco pakati panu; ndipo Israyeli wonse adzamva, nadzaopa.

22. Munthu akakhala nalo cimo loyenera imfa, kuti amuphe, ndipo wampacika;

23. mtembo wace usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopacikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 21