Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 18:12-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Popeza ali yense wakucita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo cifukwa ca zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu.

13. Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu.

14. Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kucita cotero.

15. Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;

16. monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu m'Horebe, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso mota waukuru uwu, kuti tingafe.

17. Ndipo Yehova anati kwa ine, Cokoma ananenaci.

18. Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m'kamwa mwace, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi.

19. Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m'dzina langa, ndidzamfunsa.

20. Koma mneneri wakucita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulira anene, kapena kunena m'dzina la milungu yina, mneneri ameneyo afe.

21. Ndipo mukati m'mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananena?

22. Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sacitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanena; mneneriyo ananena modzikuza, musamuopa iye.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 18