Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 14:7-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika ciboda: ngamila, ndi ka'ulu, ndi mbira, popezazibzikula, komazosagawanika ciboda, muziyese zodetsa;

8. ndi nkhumba, popeza igawanika ciboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.

9. Mwa zonse ziri m'madzi muyenera kumadya izi: ziri zonse ziri nazo zipsepse ndi mamba, zimenezi muyenera kumadya;

10. koma ziri zonse zopanda zipsepse kapena mamba musamadya; muziyese zonyansa.

11. Mbalame zosadetsazonse muyenera kumadya.

12. Koma izi ndi zimene simuyenera kumadya: mphungu, ndi nkhwazi, ndi cikambi,

13. ndi kamtema, ndi mphamba, ndi muimba monga mwa mtundu wace;

14. ndi khungubwe ali yense monga mwa mtundu wace;

15. ndi nthiwatiwa, ndi cipudo, ndi kakoa, ndi kabawi monga mwa mtundu wace;

16. ndi nkhutukutu, ndi mancici, ndi tsekwe;

17. ndi bvuwo, ndi dembu, ndi nswankhono;

18. ndi iodwa, ndi cimeza, monga mwa mtundu wace, ndi sadzu, ndi mleme.

19. Ndipo zokwawa zonse zakuuluka muziyesa zonyansa; musamazidya.

20. Mbalame zonse zosadetsa muyenera kumadya.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 14