7. Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika ciboda: ngamila, ndi ka'ulu, ndi mbira, popezazibzikula, komazosagawanika ciboda, muziyese zodetsa;
8. ndi nkhumba, popeza igawanika ciboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.
9. Mwa zonse ziri m'madzi muyenera kumadya izi: ziri zonse ziri nazo zipsepse ndi mamba, zimenezi muyenera kumadya;
10. koma ziri zonse zopanda zipsepse kapena mamba musamadya; muziyese zonyansa.
11. Mbalame zosadetsazonse muyenera kumadya.
12. Koma izi ndi zimene simuyenera kumadya: mphungu, ndi nkhwazi, ndi cikambi,
13. ndi kamtema, ndi mphamba, ndi muimba monga mwa mtundu wace;
14. ndi khungubwe ali yense monga mwa mtundu wace;
15. ndi nthiwatiwa, ndi cipudo, ndi kakoa, ndi kabawi monga mwa mtundu wace;
16. ndi nkhutukutu, ndi mancici, ndi tsekwe;