Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 10:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse ziri m'mwemo ndi zace za Yehova Mulungu wanu.

15. Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino.

16. Potero dulani khungu la mitima yanu, ndipo musamapulukiranso.

17. Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye ya ambuye; Mulungu wamkuru, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira cokometsera mlandu.

18. Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa cakudya ndi cobvala.

19. M'mwemo mukondane naye mlendo; popeza munali alendo m'dziko la Aigupto.

20. Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire Iyeyo; mummamatire iye, ndi kulumbira pa dzina lace.

21. Iye ndiye lemekezo lanu, Ive ndiye Mulungu wanu, amene anacita nanu zazikuru ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.

22. Makolo anu anatsikira ku Aigupto ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri; ndipo Yehova Mulungu wanu anakusandulizani tsopano mucuruke ngati nyenyezi za kumwamba.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 10