Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 1:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo munadandaula m'mahema mwanu, ndi kuti, Popeza anatida Yehova, iye anatiturutsa m'dziko la Aigupto, kutipereka m'manja mwa Aamori, ationonge.

28. Tikwere kuti? abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo akulu ndi atali akuposa ife; midzi ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.

29. Pamenepo ndinati kwa inu, Musamaopsedwa, musamacita mantha nao.

30. Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakucitirani m'Aigupto pamaso panu;

31. ndi kucipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wace wamwamuna, m'njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m'malo muno.

32. Koma m'cinthu ici simunakhulupirira Yehova Mulungu wanu,

33. amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi mota usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 1