Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 5:22-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo inu mwana wace, Belisazara inu, simunadzicepetsa m'mtima mwanu, cinkana munazidziwa izi zonse;

23. koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yace kwa inu; ndi inu ndi akuru anu, akazi anu ndi akazi anu ang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolidi, yamkuwa, yacitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona, kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwace muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamcitira ulemu.

24. Pamenepo nsonga ya dzanja inatumidwa kucokera pamaso pace, nililembedwa lembali.

25. Ndipolembalolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL UF ARSIN.

26. Kumasulira kwace kwa mau awa ndi uku: MENE, Mulungu anawerenga ufumu wanu, nautha.

27. TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera.

28. PERES, ufumu wanu wagawika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.

29. Pamenepo Belisazara analamulira, ndipo anabveka Danieli cibakuwa, ndi unyolo wagolidi m'khosi mwace, nalalikira za iye kuti ndiye wolamulira wacitatu m'ufumumo.

30. Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa.

31. Ndipo Dariyo Mmedi analandira ufumuwo ali wa zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri.

Werengani mutu wathunthu Danieli 5