Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 2:47-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

47. Mfumu inamyankha Danieli, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wobvumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kubvumbulutsa cinsinsi ici.

48. Pamenepo mfumu inasandutsa Danieli wamkuru, nimpatsa mphatso zazikuru zambiri, namlamuliritsa dera lonse la ku Babulo; nakhala iye kazembe wamkuru wa anzeru onse a ku Babulo.

49. Pamenepo Danieli anapempha mfumu, ndipo anaika Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, ayang'anire nchito za dera la ku Babulo. Koma Danieli anakhala m'bwalo la mfumu.

Werengani mutu wathunthu Danieli 2