Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 10:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka cacitatu ca Koresi mfumu ya Perisiya, cinabvumbulutsidwa cinthu kwa Danieli, amene anamucha Belitsazara; ndipo cinthuco ncoona, ndico nkhondo yaikuru; ndipo anazindikira cinthuco, nadziwa masomphenyawo.

2. Masiku aja ine Danieli ndinali kulira masabata atatu amphumphu,

3. Cakudya cofunika osacidya ine, nyama kapena vinyo zosapita pakamwa panga, osadzola ine konse, mpaka anakwaniridwa masabata atatu amphumphu,

4. Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi woyamba, pokhala ine m'mphepete mwa mtsinje waukuru, ndiwo Hidikeli,

5. ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wobvala bafuta, womanga m'cuuno ndi golidi woona wa ku Ufazi;

6. thupi lace lomwe linanga berulo, ndi nkhope yace ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ace ngati nyali zamoto, ndi manja ace ndi mapazi ace akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ace kunanga phokoso la aunyinji.

Werengani mutu wathunthu Danieli 10