Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 7:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ambuye Yehova anandionetsa cotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa maudzu a cibwereza; ndipo taonani, ndico cibwereza atawasengera mfumu.

2. Ndipo kunacitika m'mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala ciriri bwanji? popeza ndiye wamng'ono.

3. Ndipo Yehova anacileka. Sicidzacitika, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Amosi 7