Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 5:20-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Kodi tsiku la Yehova silidzakhala la mdima, si la kuunika ai? lakuda bii, lopanda kuwala m'menemo?

21. Ndidana nao, ndinyoza madyerero anu, sindidzakondwera nao masonkhano anu oletsa.

22. Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndinsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.

23. Mundicotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva mayimbidwe a zisakasa zanu.

24. Koma ciweruzo ciyende ngati madzi, ndi cilungamo ngati mtsinje wosefuka.

25. Ngati munabwera nazo kwa Ine nsembe zophera ndi zaufa zaka makumi anai m'cipululu, inu nyumba ya Israyeli?

26. Inde mwasenza hema wa mfumu yanu, ndi tsinde la mafano anu, nyenyezi ya mlungu wanu, amene mudadzipangira.

27. M'mwemo ndidzakutengani kumka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lace ndiye Mulungu wa makamu.

Werengani mutu wathunthu Amosi 5