Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 4:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndinakukanthani ndi cinsikwi ndi cinoni; minda yanu yocuruka yamipesa, ndi yamikuyu, ndi yaazitona, yaonongeka ndi cirimamine; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

10. Ndinatumiza mliri pakati panu monga m'Aigupto; anyamata anu ndawapha ndi lupanga, ndi kutenga akavalo anu; ndipo ndinakweretsa kununkha kwa cigono canu kufikitsa kumphuno kwanu; ikoma simunabwerera kudzakwa Ine, ati Yehova.

11. Ndinagubuduza ena mwa inu, monga umo Mulungu anagubuduzira Sodomu ndi Gomora; ndipo inu munali ngati muuni wofumulidwa kumoto; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

12. Cifukwa cace ndidzatero nawe, Israyeli; popeza ndidzakucitira ici, dzikonzeretu kukomana ndi Mulungu wako, Israyeli.

13. Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ace, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lace ndiye Yehova Mulungu wamakamu.

Werengani mutu wathunthu Amosi 4