Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 2:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. nagona pansi pa zopfunda za cikole ku maguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.

9. Koma ndinaononga Ine pamaso pa Aamori, amene msinkhu wao unanga msinkhu wa mikungudza, nakhala nayo mphamvu ngati thundu; koma ndinaononga zipatso zao m'mwamba, ndi mizu yao pansi.

10. Ndipo ndinakukwezani kucokera m'dziko la Aigupto, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'cipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale colowa canu.

11. Ndipo ndinaukitsa mwa ana anu aneneri, ndi mwa anyamata anu Anaziri. Si momwemo, inu ana a Israyeli, ati Yehova?

12. Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera.

13. Taonani, ndidzakupsinjani m'malo mwanu, monga lipsinja gareta lodzala ndi mitolo fwa.

14. Ndipo populumukirapo padzasowera waliwiro, ndi wamphamvu; sadzalimbikitsa mphamvu yace, ndi ngwazi siidzapulumutsa moyo wace;

Werengani mutu wathunthu Amosi 2