1. Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa:—Atero Davide mwana wa Jese,Atero munthu wokwezedwa,Ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo,Ndi mwini masalmo wokoma wa Israyeli:
2. Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine,Ndi mau ace anali pa lilime langa,
3. Mulungu wa Israyeli anati,Thanthwe la Israyeli Gnalankhula ndi ine;Kudzakhala woweruza anthu molungama;Woweruza m'kuopa Mulungu.
4. Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, poturuka dzuwa,M'mawa mopanda mitambo;Pamene msipu uphuka kuturuka pansi,Cifukwa ca kuwala koyera, italeka mvula.