Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 12:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Pa mudzi wina panali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka.

2. Wolemerayo anali nazo zoweta zazing'ono ndi zazikuru zambiri ndithu;

3. koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ace. Kanadyako cakudya cace ca iye yekha, kanamwera m'cikho ca iye yekha, kanagona pa cifukato cace, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wace wamkazi.

4. Ndipo kwa wolemerayo kunafika mlendo, ndipo iye analeka kutengako mwa zoweta zace zazing'ono ndi zazikuru, kuphikira mlendo amene anafika kwa iye, koma anatenga mwana wa nkhosa wa wosaukayo, naphikira munthu amene anafika kwa iye.

5. Pamenepo mkwiyo wa Davide unayaka ndithu pa munthuyo, nati kwa Natani, Pali Yehova, munthu amene anacita ici, ayenera kumupha;

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 12