Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 9:23-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zace Mulungu adazilonga m'mtima mwace.

24. Nabwera nao munthu yense mtulo wace, zipangizo zasiliva, ndi zipangizo zagolidi, zobvala, ndi zobvala za nkhondo, ndi zonunkhira, akavalo, ndi nyuru; momwemo caka ndi caka.

25. Ndipo Solomo anali nazo zipinda zikwi zinai za akavalo ndi magareta, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'toidzi ya magareta, ndi m'Yerusalemu kwa mfumu.

26. Ndipo analamulira mafumu onse kuyambira ku Firate kufikira ku dziko la Afilisti, ndi ku malire a ku Aigupto.

27. Ndipo mfumu inacurukitsa siliva m'Yerusalemu ngati miyala; ndi mikungudza anailinganiza ndi mikuyu iri kumadambo kucuruka kwace.

28. Ndipo anakamtengera Solomo akavalo ku Aigupto, ndi ku maiko onse.

29. Macitidwe ena tsono a Solomo, oyamba ndi otsiriza, salembedwa kodi m'buku la mau a Natani mneneri ndi m'zonenera za Ahiya wa ku Silo, ndi m'masomphenya a Ido mlauli za Yerobiamu mwana wa Nebati?

30. Ndipo Solomo anakhala mfumu ya Israyeli yense m'Yerusalemu zaka makumi anai.

31. Nagona Solomo pamodzi ndi makolo ace, naikidwa m'mudzi wa Davide atate wace; ndipo Rehabiamu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 9