Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 8:16-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Momwemo nchito yonse ya Solomo inakonzekeratu tsiku lakuika maziko a nyumba ya Yehova, mpaka anaitsiriza.

17. Pamenepo Solomo anamuka ku Ezioni Geberi, ndi ku Eloti pambali pa nyanja, m'dziko la Edomu.

18. Ndipo Huramu anamtumizira zombo, ndi amarinyero ace, ndi anyamata akudziwa za m'nyanja; ndipo anamuka pamodzi ndi anyamata a Solomo ku Ofiri, natengako matalente mazana anai mphambu makumi asanu a golidi, nabwera nao kwa Solomo mfumu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 8