Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 8:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene anamanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba yace yace,

2. Solomo anamanga midzi imene Huramu adampatsa, nakhalitsamo ana a Israyeli.

3. Ndipo Solomo anamuka ku Hamati Zoba, naugonjetsa.

4. Ndipo anamanga Tadimori m'cipululu, ndi midzi yonse yosungiramo cuma, imene anaimanga m'Hamati.

5. Anamanganso Betihoroni wa kumtunda, ndi Betihoroni wa kunsi, midzi ya malinga yokhala nao malinga, zitseko, ndi mipiringidzo;

6. ndi Balati, ndi midzi yonse yosungiramo cuma anali nayo Solomo, ndi midzi yonse ya magareta ace, ndi midzi ya apakavalo ace, ndi zonse anazifuna Solomo kuzimanga zomkondweretsa m'Yerusalemu, ndi m'Lebano, ndi m'dziko lonse la ufumu wace.

7. Ndipo anthu onse otsala mwa Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi, osati Aisrayeli,

8. mwa ana ao otsala m'dziko pambuyo pao, amene ana a Israyeli sanawatha, mwa iwowa Solomo anawacititsa thangata mpaka lero lino.

9. Koma mwa ana a Israyeli Solomo sanawayesa akapolo omgwirira nchito; koma iwowa anali anthu a nkhondo, akazembe ace akuru, ndi akuru a magareta ace, ndi apakavalo ace.

10. Amenewa anali akuru a akapitao a mfumu Solomo, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu akulamulira anthu.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 8