Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 4:14-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Anapanganso maphaka, napanga mbiya zamphwamphwa khumi pamwamba pa maphaka;

15. thawale limodzi ndi ng'ombe khumi ndi ziwiri pansi pace.

16. Miphika yomwe, ndi zoolera, ndi mitungo, ndi zipangizo zace zonse, Huramu Abi anazipangira mfumu Solomo, kuzipangira nyumba ya Yehova, za mkuwa wonyezimira.

17. Mfumuyi inaziyenga pa cidikha ca ku Yordano, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zereda.

18. Ndipo Solomo anazipanga zipangizo izi zonse zocurukadi, pakuti kulemera kwace kwa mkuwa sikunayeseka.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 4