Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 21:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. taonani, Yehova adzakantha anthu anu, ndi ana anu, ndi akazi anu, ndi cuma canu conse, makanthidwe akuru;

15. ndipo mudzadwala kwakukuru nthenda yamatumbo, mpaka matumbo anu adzaturuka cifukwa ca nthendayi tsiku ndi tsiku.

16. Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi;

17. ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda cuma conse cinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ace omwe, ndi akazi ace, osamsiyira mwana, koma Yehoahazi yekha mwana wace wamng'ono.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 21