Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 17:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akuru a zikwi; Adina wamkuru, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;

15. ndi wotsatana naye mkuru Yohanani, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu;

16. ndi wotsatana naye Amasiya mwana wa Zikri, wodzipereka kwa Yehova mwaufulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana awiri;

17. ndi a Benjamini: Eliyada ngwazi yamphamvu, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri ogwira mauta ndi zikopa;

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 17