Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 17:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehosafati mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace, nadzilimbitsa kuyambana ndi Israyeli.

2. Naika ankhondo m'midzi yonse yamalinga ya Yuda, naika aboma m'dziko la Yuda, ndi m'midzi ya Efraimu, imene adailanda Asa atate wace.

3. Ndipo Yehova anali ndi Yehosafati, popeza anayenda m'njira zace zoyamba za kholo lace Davide, osafuna Abaala;

4. koma anafuna Mulungu wa kholo lace nayenda m'malamulo ace, osatsata macitidwe a Israyeli.

5. Cifukwa cace Yehova anakhazikitsa ufumuwo m'dzanja lace, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamcurukira cuma ndi ulemu.

6. Ndi mtima wace unakwezeka m'njira za Yehova; anacotsanso misanje ndi zifanizo m'Yuda.

7. Caka cacitatu ca ufumu wace anatuma akalonga ace, ndiwo Benihayili, ndi Obadiya, ndi Zekariya, ndi Netaneli, ndi Mikaya, aphunzitse m'midzi ya Yuda;

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 17