Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 16:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, cifukwa cace khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.

8. Nanga Akusi ndi Alubi, sanakhala khamu lalikurukuru, ndi magareta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m'dzanja mwanu?

9. Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwacita copusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.

10. Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m'kaidi; pakuti adapsa mtima naye cifukwa ca ici. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.

11. Ndipo taonani, zocita Asa, zoyamba ndi zotsiriza, zalembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israyeli.

12. Ndipo Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mpham bu zisanu ndi zitatu, anadwala nthenda ya mapazi, nikuladi nthendayi; koma podwala iye sanafuna Yehova, koma asing'anga.

13. Nagona Asa ndi makolo ace, namwalira atakhala mfumu zaka makumi anai.

14. Ndipo anamuika m'manda ace adadzisemerawo m'mudzi wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundu mitundu, monga mwa makonzedwe a osanganiza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 16