Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 11:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehabiamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisrayeli kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu.

2. Koma mau a Yehova anadza kwa Semaya munthu wa Mulunguyo, ndi kuti,

3. Lankhula ndi Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti,

4. Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense ku nyumba yace; pakuti cinthu ici cifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobiamu.

5. Ndipo Rehabiamu anakhala m'Yerusalemu, namanga midzi yolimbikiramo m'Yuda.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 11