Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 11:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehabiamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisrayeli kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu.

2. Koma mau a Yehova anadza kwa Semaya munthu wa Mulunguyo, ndi kuti,

3. Lankhula ndi Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti,

4. Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense ku nyumba yace; pakuti cinthu ici cifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobiamu.

5. Ndipo Rehabiamu anakhala m'Yerusalemu, namanga midzi yolimbikiramo m'Yuda.

6. Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekoa,

7. ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu,

8. ndi Gati, ndi Maresa, ndi Zifi,

9. ndi Adoraimu, ndi Lakisi, ndi Azeka,

10. ndi Zora, ndi Ayaloni, ndi Hebroni; ndiyo midzi yamalinga ya m'Yuda ndi Benjamini.

11. Ndipo analimbitsa malingawo, naikamo atsogoleri, ndi cakudya cosungikiratu, ndi mafuta, ndi lvinyo.

12. Ndi m'midzi iri yonse anaikamo zikopa ndi mikondo, nailimbitsa cilimbitsire. Ndipo Yuda ndi Benjamini anakhala ace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 11