Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mbiri 1:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. nzeru ndi cidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso cuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhala nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.

13. Momwemo Solomo anadza ku Yerusalemu kucokera ku msanje uli ku Gibeoni, ku khomo la cihema cokomanako; ndipo anacita ufumu pa Israyeli.

14. Ndipo Solomo anasonkhanitsa magareta ndi apakavalo, nakhala nao magareta cikwi cimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magareta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.

15. Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golidi zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza icuruke ngati mikuyu yokhala kucidikha.

16. Ndi akavalo amene Solomo anali nao anafuma ku Aigupto; amalonda a mfumu anawalandira magulu magulu, gulu liri lonse mtengo wace.

17. Ndipo anatenga naturuka nalo gareta ku Aigupto mtengo wace masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wace zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemo anawaturutsira mafumu onse a Ahiti, ndi mafumu a Aramu, ndi dzanja lao.

Werengani mutu wathunthu 2 Mbiri 1