Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 6:31-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Nati iye, Andilange Mulungu naonjezeko, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati uti ukhale pa iye lero lino.

32. Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwace, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kucotsa mutu wanga? taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi citseko. Kodi mapazi a mbuye wace samveka dididi pambuyo pace?

33. Akali cilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, coipa ici cicokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova?

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 6