Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 20:17-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kumka ku Babulo, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.

18. Nadzatenga ena a ana ako oturuka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'cinyumba ca mfumu ya Babulo.

19. Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi coonaeli zikakhala masiku anga?

20. Macitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yace yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mcera, nautengera mudzi madzi, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

21. Nagona Hezekiya ndi makolo ace; nakhala mfumu m'malo mwace Manase mwana wace.

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 20