1. Caka cacisanu ndi ciwiri ca Yehu, Yoasi analowa ufumu wace; nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la mai wace ndiye Zibiya wa ku Beereseba.
2. Ndipo Yoasi anacita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ace onse, m'mene anamlangizira wansembe Yehoyada.
3. Koma misanje sanaicotsa; anthu anapherabe nsembe, nafukiza komisanje.