Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Mafumu 1:16-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli kufunsira mau ace? Cifukwa cace sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

17. Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwace caka caciwiri ca Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.

18. Macitidwe ace ena tsono adawacita Ahaziya, kodi salembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

Werengani mutu wathunthu 2 Mafumu 1