Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 25:26-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Cifukwa cace tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera cilango ndi dzanja la inu nokha, cifukwa cace adani anu, ndi iwo akufuna kucitira mbuye wanga coipa, akhale ngati Nabala.

27. Ndipo mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga.

28. Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka coipa masiku anu onse.

29. Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga coturuka m'coponyera mwala.

30. Ndipo kudzali, pamene Yehova anacitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israyeli;

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 25