Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 24:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali, pakubwerera Sauli potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku cipululu ca Engedi.

2. Tsono Sauli anatenga anthu zikwi zitatu osankhika pakati pa Aisrayeli onse, namuka kukafuna Davide ndi anthu ace m'matanthwe a zinkhoma.

3. Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Sauli analowa kuti akapfunde mapazi ace. Ndipo Davide ndi anyamata ace analikukhala m'kati mwa phangamo,

4. Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamcitira iye cokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli mobisika.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 24