Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 21:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo Davide ananyamuka, nathawa tsiku lomwelo cifukwa ca kuopa Sauli, namuka kwa Akisi mfumu ya ku Gati.

11. Ndipo anyamata a Akisi ananena naye, Uyu si Davide mfumu ya dzikolo kodi? Sanathirirana mang'ombe za iye kodi m'magule ao, ndi kuti,Sauli anapha zikwi zace,Koma Davide zikwi zace zankhani?

12. Ndipo Davide anasunga mau awa mumtima mwace, naopa kwambiri Akisi mfumu ya Gati.

13. Nasanduliza makhalidwe ace pamaso pao, nadzionetsera m'manja mwao ngati wamisala, nangolembalemba pa zitseko za cipata, nakhetsa dobvu lace pa ndebvu yace.

14. Tsono Akisi ananena ndi anyamata ace, Taonani, mupenya kuti munthuyo ngwa misala; mwabwera naye kwa ine cifukwa ninji?

15. Kodi ndisowa anthu amisala kuti mwabwera ndi uyu kuti akhale wamisala pamaso panga? Kodi uyu adzalowa m'nyumba mwanga?

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 21