6. Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pacaka ya banja lao lonse.
7. Tsono akati, Cabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundicitira coipa.
8. Cifukwa cace ucitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamcititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli coipa ciri conse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?
9. Ndipo Jonatani anati, lai ndi pang'ono ponse; ine ndikadziwa konse kuti atate wanga anatsimikiza mtima kukucitira coipa, sindidzadziwitsa iwe kodi?