Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 16:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo uitane Jese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza cimene uyenera kucita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakuchulira dzina lace.

4. Ndipo Samueli anacita cimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akuru a mudziwo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi?

5. Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Jese ndi ana ace, nawaitanira kunsembeko.

6. Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang'ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pace.

7. Koma Yehova ananena ndi Samueli, Vsayang'ane nkhope yace, kapena kutalika kwa msinkhu wace, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana cooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.

8. Pamenepo Jese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samueli. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankha.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 16