Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 16:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Iwe ukuti ulire cifukwa ca Sauli nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israyeli? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Jese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ace.

2. Ndipo Samueli anati, Ndikamuka bwanji? Sauli akacimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng'ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova.

3. Ndipo uitane Jese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza cimene uyenera kucita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakuchulira dzina lace.

4. Ndipo Samueli anacita cimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akuru a mudziwo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi?

5. Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Jese ndi ana ace, nawaitanira kunsembeko.

6. Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang'ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pace.

7. Koma Yehova ananena ndi Samueli, Vsayang'ane nkhope yace, kapena kutalika kwa msinkhu wace, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana cooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.

8. Pamenepo Jese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samueli. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankha.

9. Pamenepo Jese anapititsapo Sama. Ndipo anati, Koma uyunso Yehova sanamsankha.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 16