Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 5:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Yoeli mkuru wao, ndi Safamu waciwiri, ndi Yanai, ndi Safati m'Basana;

13. ndi abale ao a; nyumba za makolo ao: Mikaeli, ndi Mesulamu, ndi Seba, ndi Yorai, ndi Yakani, ndi Ziya, ndi Eberi; asanu ndi awiri.

14. Awa ndi ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Gileadi, mwana wa Mikaeli, mwana wa Yesisai, mwana wa Yado, mwana wa Buzi,

15. Ahi mwana wa Abdieli, mwana wa Guni, ndiye mkulu wa nyumba za makolo ao.

16. Ndipo anakhala m'Gileadi m'Basana, ndi m'midzi yace, ndi podyetsa pace ponse pa Saroni, mpaka malire ao.

17. Onsewo anawerengedwa monga mwa mabuku a cibadwidwe cao, masiku a Yotamu mfumu ya Yuda, ndi m'masiku a Yerobiamu mfumu ya Israyeli.

18. Ana a Rubeni, ndi a Gadi, ndi limodzi la magawo awiri a pfuko la Manase, ngwazi, amuna akugwira cikopa ndi lupanga, ndi kuponya mibvi, ozerewera nkhondo, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zinai mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi akuturuka kunkhondo.

19. Ndipo anagwirana nkhondo ndi Ahagari, ndi Yet uri, ndi Nafisi, ndi Nodabu.

20. Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagari anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anapfuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira iye.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 5