Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 3:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Anambadwira asanu ndi mmodzi m'Hebroni; ndi pomwepo anakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri, ndi miyezi isanu ndi iwiri; ndi m'Yerusalemu anakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zitatu.

5. Ndipo ombadwira m'Yerusalemu ndi awa: Simeya, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomo, anai a Batisuwa mwana wamkazi wa Amieli;

6. ndi Ibara, ndi Elisama, ndi Elifeleti,

7. ndi Noga, ndi Nefegi, ndi Yafiya,

8. ndi Elisama, ndi Eliada, ndi Elifeleti, asanu ndi anai.

9. Onsewa ndiwo ana a Davide, pamodzi ndi ana a akazi ang'ono; ndipo Tamara ndiye mlongo wao.

10. Ndipo mwana wa Solomo ndiye Rehabiamu, Abiya mwana wace, Asa mwana wace, Yeo hosafati mwana wace,

11. Yoramu mwana wace, Ahaziya mwana wace, Yoasi mwana wace,

12. Amaziya mwana wace, Azariya mwana wace, Yotamu mwana wace,

13. Ahazi mwana wace, Hezekiya mwana wace, Manase mwana wace,

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 3