Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 29:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomo yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo nchitoyi ndi yaikuru, pakuti cinyumbaci siciri ca munthu, koma ca Yehova Mulungu.

2. Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golidi wa zija zagolidi ndi siliva wa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, citsulo ca zija zacitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawanga mawanga, ndi miyala ya mtengo wace ya mitundu mitundu ndi miyala yansangalabwe yocuruka.

3. Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, cuma cangacanga ca golidi ndi siliva ndiri naco ndicipereka ku nyumba ya Mulungu wanga, moenjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;

4. ndico matalente zikwi zitatu za golidi, golidi wa Ofiri; ndi matalente zikwi zisanu ndi ziwiri a siliva woyengetsa, kumamatiza nazo makoma a nyumbazi;

5. golidi wa zija zagolidi, ndi siliva wa zija zasiliva, ndi za nchito ziri zonse akuzipanga manja a amisiri. Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira kwa Yehova lero line?

6. Pamenepo akuru a nyumba za makolo, ndi akuru a mafuko a Israyeli, ndi akuru a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira nchito ya mfumu, anapereka mwaufulu,

7. napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golidi matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi citsulo matalente zikwi zana limodzi.

8. Ndipo amene anali nayo miyala ya mtengo wace anaipereka ku cuma ca nyumba ya Yehova, mwa dzanja la Yehieli Mgerisoni.

9. Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi cimwemwe cacikuru.

10. Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israyeli, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.

11. Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi cifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi pa dziko lap ansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.

12. Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo mucita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikuru; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 29