Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 27:15-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Wakhumi ndi ciwiri wa mwezi wakhumi ndi ciwiri ndiye Heledai Mnetofati wa Otiniyeli; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

16. Koma oyang'anira mafuko a lsrayeli ndi awa: wa Arubeni mtsogoleri wao ndiye Eliezeri mwana wa Zikiri; wa Asimeoni, Sefatiya mwana wa Maaka;

17. wa Alevi, Hasabiya mwana wa Kemueli; wa Aroni, Zadoki;

18. wa Yuda, Elihu mbale wina wa Davide; wa Isakara, Omri mwana wa Mikaeli;

19. wa Zebuluni, Isimaya mwana wa Obadiya; wa Nafitali, Yeremoti mwana wa Azrieli;

20. wa ana a Efraimu, Hoseya mwana wa Azaziya; wa pfuko la Manase logawika pakati, Yoeli mwana wa Pedaya;

21. wa pfuko la Manase logawika pakati m'Gileadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yasiyeli mwana wa Abineri;

22. wa Dani, Azareli mwana wa Yerohamu. Awa ndi akazembe a mapfuko a Israyeli.

23. Koma Davide sanawerenga iwo a zaka makumi awiri ndi ocepapo, pakuti Yehova adati kuti adzacurukitsa Israyeli ngati nyenyezi za kuthambo.

24. Yoabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsiriza; ndi mkwiyo unagwera Israyeli cifukwa ca ici, ndipo ciwerengo cao sicinalembedwa m'buku la mbiri ya mfumu Davide.

25. Ndipo woyang'anira cuma ca mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyeli, ndi woyang'anira wa cuma ca m'minda, m'mizinda ndi m'miraga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;

26. ndi woyang'anira iwo akugwira nchito ya m'munda yakulima nthaka ndiye Ezri mwana wa Kelubi;

27. ndi woyang'anira minda yamphesa ndiye Simeyi Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yamphesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifimi;

28. ndi woyang'anira mitengo yaazitona, ndi yamikuyu yokhala kuzidikha kunsi, ndiye Baala Hanani Mgederi; ndi woyang'anira zosungiramo mafuta ndiye Yoasi;

29. ndi woyang'anira ng'ombe zakudya m'Saroni ndiye Sitirai Msaroni; ndi woyang'anira ng'ombe za m'zigwa ndiye Safabi mwana wa Adilai;

30. ndi woyang'anira ngamira ndiye Obili M-israyeli; ndi woyang'anira aburu ndiye Yedeya Mmeronoti;

31. ndi woyang'anira zoweta zazing'ono ndiye Yazizi Mhagiri, Onsewa ndiwo akuru a zolemera zace za Davide.

32. Ndipo Yonatani atate wace wina wa Davide anali phungu, munthu wanzeru ndi mlembi; ndi Yehieli mwana wa Hakimoni anakhala ndi ana a mfumu;

33. ndi Ahitofeli anali phungu wa mfumu, ndi Husai M-ariki anali bwenzi la mfumu;

34. ndi wotsatana ndi Ahitofeli, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yoabu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 27