Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 26:4-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Obedi Edomu anali nao ana, woyamba Semaya, waciwiri Yozabadi, wacitatu Yowa, wacinai Sakara, wacisanu Netaneli,

5. wacisanu ndi cimodzi Amiyeli, wacisanu ndi ciwiri Isakara, wacisanu ndi citatu Peuletai; pakuti Mulungu adamdalitsa.

6. Kwa Semaya mwana wace yemwe kunabadwa ana, akulamulira nyumba ya atate wao; pakuti anali ngwazi zamphamvu.

7. Ana a Semaya: Otini, ndi Refaeli, ndi Obedi, Elzabadi, amene abale ao ndiwo odziwa mphamvu, Elihu, ndi Semakiya.

8. Onsewa ndiwo a ana a Obedi Edomu; iwo ndi ana ao, ndi abale ao, anthu odziwa mphamvu yakutumikira, makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri a Obedi Edomu.

9. Ndi Meselemiya anali ndi ana, ndi abale odziwa mphamvu khumi mphambu asanu ndi atatu.

10. Hosa yemwe wa ana a Merari anali ndi ana, wamkuru ndi Simri; pakuti ngakhale sanali wobadwa woyamba, atate wace anamuyesa wamkuru;

11. waciwiri Hilikiya, wacitatu Tebaliya, wacinai Zekariya; ana ndi abale onse a Hosa ndiwo khumi ndi atatu.

12. Mwa iwowa munali magawidwe a odikira, mwa akulu a amuna akucita udikiro wao, monga abale ao, kutumikira m'nyumba ya Yehova.

13. Ndipo anacita maere ang'ono ndi akuru, monga mwa nyumba za makolo ao, kucitira zipata zonse.

14. Ndi maere a kum'mawa anagwera Selemiya. Ndipo anacitira maere Zekariya mwana wace, phungu wanzeru, ndi maere anamgwera kumpoto;

15. Obedi Edomu kumwela, ndi ana ace nyumba ya akatundu.

16. Supimu ndi Hosa kumadzulo, ku cipata ca Saleketi, ku mseu wokwerapo, udikiro pandunji pa udikiro.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 26