Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 26:13-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo anacita maere ang'ono ndi akuru, monga mwa nyumba za makolo ao, kucitira zipata zonse.

14. Ndi maere a kum'mawa anagwera Selemiya. Ndipo anacitira maere Zekariya mwana wace, phungu wanzeru, ndi maere anamgwera kumpoto;

15. Obedi Edomu kumwela, ndi ana ace nyumba ya akatundu.

16. Supimu ndi Hosa kumadzulo, ku cipata ca Saleketi, ku mseu wokwerapo, udikiro pandunji pa udikiro.

17. Kum'mawa kunali Alevi asanu ndi mmodzi, kumpoto anai tsiku ndi tsiku, kumwela anai tsiku ndi tsiku, ndi a nyumba ya akatundu awiri ndi awiri.

18. Ku Parabara kumadzulo anai kumseu, ndi awiri ku Parabara.

19. Awa ndi magawidwe a odikira; a ana a Akora, ndi a ana a Merari.

20. Ndipo wa Alevi, Ahiya anayang'anira cuma ca nyumba ya Mulungu, ndi cuma ca zopatulika.

21. Ana a Ladani: ana a Ladani a Agerisoni, akuru a nyumba za makolo a Ladani Mgerisoni, Yehieli.

22. Ana a Yehieli: Zetamu ndi Yoeli mbale wace, oyang'anira cuma ca nyumba ya Yehova.

23. A Amirami, a Aizari, a Ahebroni, a Auziyeli;

24. ndi Sebueli mwana wa Gerisomu, mwana wa Mose, ndiye mkuru woyang'anira zuma.

25. Ndi abale ace a Eliezeri: Rehabiya mwana wace, ndi Yesava mwana wace ndi Yorramu mwana wace, ndi Zikiri mwana wace, ndi Selomoti mwana wace.

26. Selomoti amene ndi abale ace anayang'anira cuma conse ca zinthu zopatulika, zimene Davide mfumu ndi akuru a nyumba za akulu, akuru a zikwi ndi mazana, adazipatula.

27. Kutenga pa zofunkha kunkhondo, anapatulako kukonzera nyumba ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 26