Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 26:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. A magawidwe a odikira a Akora: Meselemiya mwana wa Kore wa ana a Asafu.

2. Ndipo Meselemiya anali ndi ana, woyamba Zekariya, waciwiri Yedyaeli, wacitatu Zebadiya, wacinai Yatiniyeli,

3. wacisanu Elamu, wacisanu ndi cimodzi Yohanana, wacisanu ndi ciwiri Elihunai.

4. Ndipo Obedi Edomu anali nao ana, woyamba Semaya, waciwiri Yozabadi, wacitatu Yowa, wacinai Sakara, wacisanu Netaneli,

5. wacisanu ndi cimodzi Amiyeli, wacisanu ndi ciwiri Isakara, wacisanu ndi citatu Peuletai; pakuti Mulungu adamdalitsa.

6. Kwa Semaya mwana wace yemwe kunabadwa ana, akulamulira nyumba ya atate wao; pakuti anali ngwazi zamphamvu.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 26