Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 24:18-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. wa makumi awiri ndi citatu Delaya, wa makumi awiri ndi cinai Miziya.

19. Awa ndi malongosoledwe ao m'utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ciweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israyeli anamlamulira.

20. Ndipo wa ana otsala a Levi: wa ana a Amiramu, Subaeli; wa ana a Subaeli, Yedeya.

21. Wa Rehabiya: wa ana a Rehabiya, mkuru ndi Isiya.

22. Wa Aizari: Selomoti; wa ana a Selomoti, Yahati.

23. Ndi wa ana a Hebroni: mkuru ndi Yeriya, waciwiri Amariya, wacitatu Yahazieli, wacinai Yekameamu.

24. Wa ana a Uziyeli, Mika; wa ana a Mika, Samiri.

25. Mbale wa Mika, Isiya; a ana a Isiya, Zekariya,

26. Ana a Merari: Mali ndi Musi; mwana wa Yaziya, Beno.

27. Ana a Merari: wa Yaziya, Beno, ndi Sohamu, ndi Sakuri, ndi Ibri.

28. Wa Mali: Eleazara, ndiye wopanda ana.

29. Wa Kisi: mwana wa Kisi, Yerameli.

30. Ndi ana a Musi: Mali, ndi Ederi, ndi Yerimoti, Awa ndi ana a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.

31. Awanso anacita maere monga abale ao ana a Aroni, pamaso pa Davide mfumu, ndi Zadoki, ndi Ahimeleki, ndi akuru a nyumba za makolo za ansembe ndi Alevi; mkuru wa nyumba za makolo monga mng'ono wace.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 24