Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 24:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. wakhumi ndi citatu Hupa, wakhumi ndi cinai Yesebeabu,

14. wakhumi ndi cisanu Biliga, wakhumi ndi cisanu ndi cimodzi Imeri,

15. wakhumi ndi cisanu ndi ciwiri Heziri, wakhumi ndi cisanu ndi citatu Hapizezi,

16. wakhumi ndi cisanu ndi cinai Petahiya, wa makumi awiri Yehezikeli,

17. wa makumi awiri ndi cimodzi Yakini, wa makumi awiri ndi ciwiri Gamuli,

18. wa makumi awiri ndi citatu Delaya, wa makumi awiri ndi cinai Miziya.

19. Awa ndi malongosoledwe ao m'utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ciweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israyeli anamlamulira.

20. Ndipo wa ana otsala a Levi: wa ana a Amiramu, Subaeli; wa ana a Subaeli, Yedeya.

21. Wa Rehabiya: wa ana a Rehabiya, mkuru ndi Isiya.

22. Wa Aizari: Selomoti; wa ana a Selomoti, Yahati.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 24