Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 22:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Nakonzeratu Davide citsulo cocuruka ca misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wocuruka wosauyesa kulemera kwace;

4. ndi mitengo yamikungudza yosaiwerenga; pakuti Asidoni ndi Aturo anabwera nayo kwa Davide mitengo yamikungudza yocuruka,

5. Ndipo Davide anati, Solomo mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikuru yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mocuruka asanamwalire.

6. Pamenepo iye anaitana Solomo mwana wace, namlangiza ammangire Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

7. Ndipo Davide anati kwa Solomo mwana wace, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 22