Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 22:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israyeli.

2. Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m'dziko la Israyeli; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu.

3. Nakonzeratu Davide citsulo cocuruka ca misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wocuruka wosauyesa kulemera kwace;

4. ndi mitengo yamikungudza yosaiwerenga; pakuti Asidoni ndi Aturo anabwera nayo kwa Davide mitengo yamikungudza yocuruka,

5. Ndipo Davide anati, Solomo mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikuru yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mocuruka asanamwalire.

6. Pamenepo iye anaitana Solomo mwana wace, namlangiza ammangire Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

7. Ndipo Davide anati kwa Solomo mwana wace, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.

8. Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wocuruka, popeza wacita nkhondo zazikuru; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 22