Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 2:13-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. ndi Jese anabala mwana wace wamwamuna woyamba Eliabu, ndi Abinadabu waciwiri, ndi Simeya wacitatu,

14. Netaneli wacinai, Radai wacisanu,

15. Ozemu wacisanu ndi cimodzi, Davide wacisanu ndi ciwiri;

16. ndi alongo ao ndiwo Zeruya ndi Abigaili. Ndi ana a Zeruya: Abisai ndi Yoabu, ndi Asaheli; atatu.

17. Ndi Abigaili anabala Amasa; ndi atate wa Amasa ndiye Yeteri M-ismayeli.

18. Ndi Kalebi mwana wa Hezroni anabala ana ndi Azuba mkazi wace, ndi Yerioti; ndipo ana ace ndiwo Yeseri, ndi Sobabu, ndi Aridoni.

19. Namwalira Azuba, ndi Kalebi anadzitengera Efrati, amene anambalira Huri.

20. Ndi Huri anabala Uri, ndi Uri anabala Bezaleli.

21. Ndipo pambuyo pace Hezroni analowa kwa mwana wamkazi wa Makiri atate wa Gileadi, amene anamtenga akhale mkazi wace, pokhala wa zaka makumi asanu ndi Gmodzi mwamunayo; ndipo mkaziyo anambalira Segubu.

22. Ndi Segubu anabala Yairi, amene anali nayo midzi makumi awiri mphambu itatu m'dziko la Gileadi.

23. Ndi Gesuri ndi Aramu analanda midzi ya Yairi, pamodzi ndi Kenati ndi miraga yace; ndiyo midzi makumi asanu ndi limodzi. Iwo onse ndiwo ana a Makiri atate wa Gileadi.

24. Ndipo atafa Hezroni m'Kalebi-Efrata, Abiya mkazi wa Hezroni anambalira Asini atate wa Tekoa.

25. Ndi ana a Yerameli mwana woyamba wa Hezroni ndiwo: woyamba Ramu, ndi Buna, ndi Oreni, ndi Ozemu, ndi Ahiya.

26. Ndipo Yerameli anali naye mkazi wina dzina lace ndiye Atara, ndiye mace wa Onamu.

27. Ndipo ana a Ramu mwana woyamba wa Yerameli ndiwo Maazi, ndi Yamini, ndi Ekeri.

28. Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri.

29. Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi.

30. Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 2