Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 15:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mudzi mwace, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.

2. Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira iye kosatha.

3. Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisrayeli onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwace adalikonzera.

4. Ndipo Davide anasonkhanitsa ana a Aroni ndi Alevi;

5. a ana a Kohati, Urieli mkuru wao, ndi abale ace zana limodzi mphambu makumi awiri;

6. a ana a Merari, Adaya mkuru wao, ndi abale ace mazana awiri mphambu makumi awiri;

7. a ana a Gerisomu, Yoeli mkuru wao, ndi abale ace zana limodzi mphambu makumi atatu;

8. a ana a Elizafana, Semaya mkuru wao, ndi abale ace mazana awiri;

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 15