Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mbiri 14:13-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo Afilisti anabwerezanso, nafalikira m'cigwamo.

14. Ndipo Davide anafunsiranso kwa Mulungu, nanena Mulungu naye, Usakwera kuwatsata, uwazungulire, nuwadzere pandunji pa mitengo ya mkandankhuku.

15. Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula kunsonga kwa mitengo ya mkandankhuku, pamenepo uturukire kunkhondo; pakuti Mulungu waturukira pamaso pako kukantha gulu la Afilisti.

16. Nacita Davide monga Yehova adamuuza, nakantha gulu la Afilisti kuyambira ku Gibeoni kufikira ku Gezeri.

17. Ndipo mbiri ya Davide inabuka m'maiko onse, nafikitsira Yehova kuopsa kwace pa amitundu onse.

Werengani mutu wathunthu 1 Mbiri 14